Bwalo la milandu m’boma la Mangochi lalamula mamuna wina wa zaka 28 zakubadwa kuti akakhale ku ndende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka zisanu ndi zinayi litamupeza olakwa pa mlandu othyola ndi kuba m’nyumba.
Malinga ndi wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergent Amina Daudi, mamunayu yemwe dzina lake ndi Sanudiya Merekaamachokera m’mudzi wa Mpandila kwa mfumu yaikulu Jalasi m’boma la Mangochi.
Sergent Daudi ati bwaloli kudzera kwa wapolisi otengera nkhani ku bwalo lamilandu ku polisi ya Namwera Constable Raphael Chitsambalinamva kuti usiku wa pa 4 mwezi uno Mereka anathyola nyumba ya a Rajab ndi kubamo katundu wa ndalama zokwana 2 hundred 80 sauzande kwacha.
Iwo ati apolisi anagwira mamunayu katundu yemwe anabayo atamupeza akugulitsidwa ndi a Gerald George pa msika wa Chiponde m’bomalo.
Mereka atavomera kuti ndi olakwa pa mlanduwu, Constable Chitsamba anapempha bwaloli kuti limupatse chilango chokhwima ndipo iye asanalandire chigamulo anapempha bwaloli kuti limumvere chisoni kaamba koti ndi koyamba kupalamula.
Popereka chigamulo chake Second Grade Magistrate Pearson Mwanyali anagwirizana ndi zomwe Constable Chitsamba anafotokoza ndipo ndi chifukwa chake anapereka chigamulo cha mtunduwu.