Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wavomereza kuti Francisco ndi Yacinta Odala a mdziko la Portugal ana omwe anakumana ndi Mai Maria wa ku Fatima atchulidwe oyera.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican mwambo wokhazikitsa awiriwa uchitika mmwezi wa May pomwenso mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu akuyembekezeka kukayendera dzikolo pa 12 ndi pa 13 mmweziwu.
Papa Yohane Paulo wachiwiri woyera anatchula ana awiriwa kuti ndi odala pa 13 May mchaka cha 2000, pa tsiku lokumbukira kuti patha zaka 83 Mai Maria wa ku Fatima atawaonekera.
Iye ati anachita izi pofuna kupereka phunziro lakuti ana nawonso atha kusanduka oyera.