Anthu makumi awiri (20) ali m’manja mwa apolisi m’boma la Ntchisi kaamba kowaganizira kuti apalamula milandu yosiyanasiyana.
Malingana ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo, Sergeant Gladson Mbumpha, anthu-wa awagwira mu sabata-yi, apolisi atakhwimitsa chitetedzo m’madera ena, monga pa msika wa pa boma, ndi wa khuwi m’bomalo.
Yemwe amatsogolera ntchito-yi ndi Detective Superintendent Getrude Mnkhondia. Iwo ati anthu-wa ndi a zaka zapakati pa 20ndi 45.
Malingana ndi a M’bumpha ina mwa milandu yomwe anthu-wa akuyenera kukayankha ku bwalo la milandu ndi yotsekula malo omwera mowa nthawi yosavomelezeka, kuchita za malonda opanda ziphatso zowayeneleza, yakuba, yogwilira ndi ina yambiri.
Padakalipano anthu-wa ali m’manja mwa apolisi ndipo akaonekera ku khoti posachedwa.