Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu 8 Afa pa Chipolowe Mdziko la India

$
0
0

Anthu asanu ndi atatu 8 afa ndipo ena ambiri avulala pa chipolowe chomwe chinabuka pakati pa apolisi ndi anthu ena omwe amachita ziwonetsero pa chisankho cha padera mdziko la India.

Malipoti a wailesi ya BBC ati apolisi anayamba kuwombera pamene anthuwa amachita chiwonetsero podana ndi ulamuliro wa dzikolo pamene amagenda komanso kusokoneza malo ochitira voti.

Padakali pano akuluakulu ena mdzikolo apempha anthu kuti anyanyale kuponya voti ndipo malipoti ati anthu amene anakaponya voti patsikuli anali 7mwa 100 aliwonse yomwe ndi nambala yotsika kwambiri poyerekeza ndi zaka za m’mbuyomu.

Patsikuli anthu okwiyawa anatentha sukulu ndi kutseka misewu ndipo ntchito zambiri pa tsikuli zinayima.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>