Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Wadzudzula Chiwembu cha Matchalitchi a Anglican Mdziko la Egypt

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse PapaFancisko wadzudzula chiwembu chomwe chachitika m’matchalitchi awiri a mpingo wa Anglican mu mzinda wa Cairo mdziko la Egypt chomwe chapha anthu 44 ndi kuvulaza anthu oposa 60.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati Papa ndi okhudzidwa kwambiri ndi chiwembuchi ndipo wapepesa mtsogoleri wa mpingo wa Anglican pa dziko lonse Papa Tawadros wachiwiri kaamba ka ngoziyi.

Chiwembuchi chachitika pamene anthu a mpingowu anasonkhana mu tchalitchi la St. George chomwe chili ku mpoto kwa mzinda wa Cairo komanso tchalitchi cha St. Mark pomwe amachita chaka cha Kanjedza.

Papa wati akupemphelera onse omwe afa komanso kuvulala pa chiwembuchi ndi onse okhudzidwa.

Malipoti ati mtsogoleri wa mpingo wa katolikayu akuyembekezeka kukayendera dziko la Egypt kumapeto a mwezi uno.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>