Mkulu wa mpingo wina pamodzi ndi anthu makumi asanu 50 ati atuluka ku ndende ina mu mzinda wa Kinshasa mdziko la Democratic Republic of Congo DRC potsatira zamtopola zomwe anthu otsatira mpingowu anakachita ku ndendeyi. Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC anthuwa anayamba kuwombera ku ndendeyi zomwe zinachititsa mkuluyi Ne Muanda Nsemi pamodzi ndi anthu enawo kuthawa. Mkuluyi yemwe ati amadzitcha mneneri anamangidwa mmwezi wa March chaka chino potsatira kusamvana komwe kunalipo pakati pa anthu a mpingo wake ndi apolisi a mdzikolo. Malinga ndi malipoti a Nsemi amafuna kuti dziko la DRC libwelere mu ulamuliro wakale wa nthawi yomwe lisanalindire ufulu wodzilamulira.
↧