Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Radio Maria Itsekera Masiku Atatu Othamanga ndi Amayi Maria Mwakathithi

$
0
0

Radio Maria Malawi lamulungu yatsekera masiku ake atatu othamanga ndi amayi Maria mwakathithi omwe inayamba lachisanu.

Ntchitoyi ayitsekera lamulungu usiku ndi mwambo wa nsembe ya misa ndipo polankhula  mkulu woona za mapologalamu ku wailesiyi Bambo Joseph Kimu wati mwambo waukulu wotsekera ntchitoyi udzachitika loweruka ku malo oyera ku Michiru mu Arch dayosizi ya Blantyre.

“Mwambo waukulu wotsekera Mariatona ukachitika ku Michiru komwe tikayambe ndi  njira ya mtanda pambuyo pake mwambo wa nsembe ya misa, kudalitsa madzi komanso kuthandiza Radio Maria Malawi,” anatero Bambo Kimu.

Cholinga cha Mariatona ameneyu ndi kupeza ndalama zosachepera 28 miliyoni kwacha yomwe cholinga chake ndi kumangira malo opemphelerapo pa goloto la amayi Maria, kukonzera zowonongeka mma transimmitter onse omwe wailesiyi ili nawo, kukonzera nyumba yowulutsira mawu ya wailesiyi ku Mangochi komanso  kugulira zida zowulitsira mawu zoyenda nazo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>