Mwambo wokondwelera kuti parish ya Bango ku Mulanje mu arch-dayosizi ya Blantyre kuti yakwanitsa zaka 50 chiyikhadzikitsileni udzachitika pa 3 mwezi wa June chaka chino.
Wapampando wa komiti yomwe ikuyendetsa mwambowu a Martha Khembo ndi omwe anena izi pofotokozera mtolankhani wathu amene amafuna kudziwa zambiri zokhudza chakachi.
Iwo ati akhristu akuyenera kudzafika mwa unyinji wawo kuti mwambowu udzakhele wopambana.