M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse papa Francisco wauza ma episikopi a mpingowu m’dziko la Italy kuti ndi bwino kulankhula mwa ufulu ngakhale zolankhulazo zitakhala kuti sizingakondweretse aliyense.
Papa Francisco amalankhula izi ku likulu la mpingo-wu potsekulira msonkhano wa nambala 70 wa ma episikopi a mpingowu a m’dzikomo.
Iye wati amakhulupilira kuti kulankhula mwachilungamo kumathandiza kaamba koti anthu sakhala ndi mpata wolankhulanso za miseche.
Polankhula wapampando wa bungwe la ma episikopili m’dzikomo Cardinal Angelo Bagnasco wapempha ma episikopi-wa kuti adzipereke pa ntchito zokweza bungwe-li.