Bwalo la milandu m’boma la Mangochi lalamula bambo wina wa zaka 50 zakubadwa kuti apereke ndalama zokwanira 1 miliyoni 8 hundred 64 sauzande 3 hundred and 86 kwacha kulephera apo akakhale ku ndende kwa miyezi makumi anayi kaamba kopezeka olakwa pa mlandu wopezeka ndi makhwala opanda chilolezo.
Bwaloli kudzera kwa wapolisi wotengera nkhani ku bwalo la milandu Inspector Effort Kamphonje linamva kuti a polisi kudzera kwa anthu a m’bomali anatsinidwa khutu kuti a Dingi Matulapansi akusunga mankhwala opanda ziphaso zowayeneleza ndipo pambuyo pake atakachita chipikisheni ku nyumba kwake anakapezadi kuti mkuluti akusungira makhwalawo ndipo nkhaniyi italowa mkhothi mpamene amupeza kuti ndi olakwa pa mulanduwu.
A Dingi Matulapansi amachokera m’mudzi mwa Mapira m’dera la mfumu yayikulu Mponda m’boma lomwelo la Mangochi.