Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse papa Francisco lero anakumana ndi m’tsogoleri wadziko la United States of America a Donald Trump.
Malingana ndi malipoti a BBC atsogoleriwa anakumana ku likulu la mpingowu ku Vatican ndipo anachita zokambirana zawo kwa mphindi makumi awiri 20.
President Trump ali pa ulendo woyendera ena mwa atsogoleri a mmayiko aku Ulaya komwe akukambirana nawo mfundo zofuna kuthana ndi zigawenga za chisilamu za Islamic State (IS).
Zina mwa zomwe atsogoleriwa akambirana ndi nkhani ya kusintha kwa nyengo ndi nkhani ya anthu omwe amalowa mdziko la America mozemba omwe amadzera mdziko la Italy.