Apolisi atatu afa ndipo anthu wamba khumi avulala mu mzinda wa Jakarta mdziko la Indonesia kaamba ka mabomba awiri omwe anaponyedwa pa malo ena okwelera bus mu mzindawo.
Malipoti a wailesi ya BBC atianthu awiri omwe anachita chiwembuchi afera pa malopo. Mmwezi wa January chaka chino zigawenga zinayi zinawombera anthu enanso anayi mchigawo chapakati cha mzinda omwewu wa Jakarta.