Anthu wamba oposera 200 ndi omwe afa mdziko la Syria kaamba ka mabomba ochokera mu ndege za asilikali a mdziko la America kuyambira pa 23 April kufikira pano.
Malinga ndi malipoti a News 24 bungwe lowona za maufulu a anthu mdzikolo litachita kafukufuku lapeza kuti mwa anthuwa makumi asanu ndi atatu 80 ndi ana komanso amayi.
Asilikali a mdziko la America anayamba kuponya mabomba mdziko la Syria mmwezi wa September chaka cha 2014 pofuna kuthana ndi gulu la zigawenga la chisilamu la Jihadists.