Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati ndi okhumudwa ndi chiwembu chomwe chachitika mu mzinda wa Manchester ku England chomwe chaphetsa anthu oposera makumi awiri ndi kuvulaza ena oposera makumi asanu.
Papa Francisco walankhula izi kudzera mu kalata yomwe walembera dziko la England ndipo wati ali limodzi mmapemphero ndi onse omwe akhudzidwa ndi chiwembuchi. Iye wati apemphelera mtendere ku mabanja onse omwe ataya ana awo pa chiwembuchi komanso magulu onse omwe akuthandiza anthu onse omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.