Amai a bungwe la Catholic Women Organization (CWO) m’dayosizi ya Zomba apereka katundu osiyanasiyana ku seminare yaikulu ya St Peter’s m’bomalo.
Poyankhula ndi Radio Maria Malawi wapampando wa bungwe-li mu dayosizi-yi mai Elizabeth Meke wati bungwe lawo lipitiliza kuthandiza seminare-yi ndichlinga choti mpingo ukhale ndi ansembe ambiri.
Iwo ati akhristu ali ndi udindo wothandiza asemino-wa pa maphunziro ndinso umoyo wawo wa tsiku ndi tsiku kaamba koti nawonso ndi anthu ngati ife tomwe.
Ndipo Dikoni Charles Danken yemwe ndi mkulu woyang’anira a semino komanso madikoni pa seminare-yi wati ophunzira ku seminare-yi ndi osangalala kaamba koti anthu ambiri amawafunira zabwino pamene amawathandiza ndi zinthu zosiyanasiyana.