Anthu asanu ndi awiri 7 afa ndipo ena avulala basi yomwe anakwera itagwa pa Mlangeni m`boma la Ntcheu.
Wofalitsa nkhani za apolisi m`bomali a Gift Matewere atsimikiza zankhaniyi ndipo ati basiyi yomwe nambala yake ndi NA 4430 ya kampani ya Premier imachokera ku Blantyre kupita ku Lilongwe .
Iwo ati dalaiva wa basiyi a Richard Nyirenda azaka 40 anapephera kukhota pamalo ena kaamba koti panthawiyo amagona zomwe zinachititsa kuti basiyo isemphe msewu ndikugwa.