Bungwe la Cooperazione Internazionale (COOPI) lati liwonetsetsa kuti likupititsa patsogolo kudzidalira kwa anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi mdziko muno.
Wamkulu wa bungweli mdziko muno mayi Ondine Tsaconas ndi omwe anena izi m’dera la mfumu yaikulu Mponda m’boma la Mangochi pamene amachita chionetsero cha chipangizo chomwe bungweli lakonza chowunika malo amene akhudzidwa ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi.
Ngati njira imodzi yokonzekeretsa anthu za ngozi zogwa mwadzidzidzi mdziko muno, bungwe la Cooperazione Internazionale (COOPI)lapanga ti ndege tomwe tikumajambula malo (mapu) omwe akumagwiritsidwa ntchito powona ngati malowo ali pachiopsezo chokhudzidwa ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi.
Wamkulu wa bungweli mdziko muno Mayi Ondine Tsaconas ati kupatula kuwona za ngozi zogwa mwadzidzidzi, bungweli limalimbikitsanso ulimi komanso kuwonetsetsa kuti anthu akukhala ndi chakudya chokwanira.
Malinga ndi mlangizi wamkulu woyang’anira za ngozi zogwa mwadzidzidzi ku bungweli a Aubrey Nyekanyeka, ntchitoyi ndiyofunika kwambiri pakuti ithandiza anthu m’mabomawa kupewa ngozi zogwa mwadzidzidzi.
Pakadali pano bungwe la COOPI likugwira ntchitoyi m’maboma a Salima ndi Mangochi koma lati likugwiranso ntchito ndi mabungwe ena m’maboma a Chikwawa, Karonga, Nsanje, Balaka komanso Dedza.
Ntchitoyi ikugwiridwa m’madera asanu ndi awiri a m’boma la Mangochi omwe ndi a mfumu Chimwala, Mponda, Namkumba, Makanjira, Namavi, Katuli komanso Chowe.
Bungwe la COOPI likugwira ntchitoyi ndi thandizo la chuma lochokera ku bungwe la European Commission for Humanitarian Aid and Civil Protection Committee (ECHO)
Bungwe laCOOPI ndi lochoka m’dziko la Italy ndipo linayamba kugwira ntchito m’dziko muno mchaka cha 1999.