Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Alangiza Ophunzira Kukonzekera Bwino Mayeso

$
0
0

Episikopi wa dayosizi ya Uppershire ya mpingo wa Anglican Ambuye Brighton Malasa analimbikitsa ophunzira a folomu folo pa sukulu ya sekondale ya Malosa m’boma la Zomba kuti akonzekere bwino pomwe akufuna kulemba mayeso a chaka chino.

A Malasa amalankhula izi pomwe ophunzira pa sukuluyi amachita mwambo wotsanzikana ndi anzawo kamba koti amaliza gawo la maphunziro awo aku sekondale. Iwo anati kukonzekera bwino mayeso kumathandiza ophunzira kuewa m’chitidwe wa chinyengo ndi kubera nthawi ya mayeso. Ambuye Brighton Malasa anati mpingo wa Anglican upitiliza kulimbikitsa ntchito za maphunziro pa sukuluyi ndi m’dziko muno.

Polankhulapo mphunzitsi wa mkulu wa sukuluyi a Nelson Mwaleanayamikira chidwi chomwe ophunzirawa akhala akuonsetsa zomwe ati zikupeleka chitsimikizo chakuti akalemba mayeso awo ophunzirawa adzachita bwino koposa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>