Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati anthu akuyenera kugwira ntchito molimbika pofuna kuthetsa mchitidwe wozembetsa anthu.
Papa amalankhula izi lamulungu pa ku likulu la mpingowu ku Vatican pomwe amachita mapemphero ndi alendo ochokera mmadera osiyanasiyana omwe anakayendera likulu la mpingo wakatolikali.
Papa wati chaka ndi chaka abambo, amayi komanso ana amakhala akuzembetsedwa ndi cholinga choti azikagwiritsidwa ntchito zosiyanasiyana zomwe zili zosayenera.
Pamenepa mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu wapempha anthu omwe anasonkhana pa malowa kuti agwirane manja pothetsa mchitidwewu.