Kumenyana kwa mphamvu kwabuka pakati pa asilikali a mdziko la Afghanistan ndi zigawenga za chisilamu za Islamic State potsatira chiwembu chomwe zigawengazi zinakachita ku ofesi ya kazembe wa dziko la Iraq mu mzinda wa Kabul.
Malipoti a wailesi ya bbc ati anthu anayi a mgulu la zigawengali ndi omwe anakachita chiwembuchi pomwe mmodzi mwa iwo anavala bomba lomwe linaphulitsidwa pa malowa ndipo ena atatuwo avulaza anthu ena omwe anali ku ofesiyi pa nthawiyo.
Chiwembuchi chachitika patadutsa sabata ziwiri pomwe dziko la Iraq limakondwelera kuti lagonjetsa gulu la zigawengali mu mzinda wa Mosul mdzikolo.