Galimoto lina lomwe woyendetsa wake sakudziwika ati lapha m’nyamata wa zaka khumi ndi zinayi (14) ndi kuvulaza ena atatu m’boma la Mangochi.
Malinga ndi wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi m’boma la Mangochi, Sergeant Amina Tepani Daudi, galimotoli lomwe linali pa liwiro la mphamvu ati linaphonya msewu ndi kuwomba anthuwa.
Malipoti ati m’nyamatayu yemwe dzina lake ndi Madalitso Isaac wafera pa malo a ngoziwo ndipo ovulalawo atengeredwa pa chipatala cha boma la Mangochi.
Galimotoli ati litawomba anthuwa, woyendetsa anathawa ndipo pakadali pano apolisi akumufunafuna. Mkuluyu akapezeka ati akayankha mlandu wolephera kukanena za ngozi ku polisi, wokanika kuthandiza anthu pa nthawi ya ngozi, woyendetsa galimoto mosasamala, komanso wochititsa imfa kaamba koyendetsa galimoto mosasamala.
Madalitso Isaac amachokera m’mudzi mwa Disi mfumu yaikulu Nsamala m’boma la Balaka.