Otumikira Radio Maria Malawi ku Zomba awalimbikitsa kuti asafooke koma kuti adzidzipeleka pa ntchito yawo.
Bambo Peter Lufeyo, otumikira mpingo wakatolika mu dayosizi ya Zomba ndi omwe anena izi utangotha m’bindikiro wa uzimu umene wailesi-yi inakonzera atumiki ake. .
Bambo Lufeyo ati kutumikira Mulungu ndi madalitso apadera ndipo anapemphanso mavolontiyawa kuti azikonda kupemphera ndi kuyeletsa mitima yawo ndi cholinga choti azitha kutumikira bwino Mulungu ali oyera mitima.
Polankhula mmalo mwa otumikira wailesiyi ku Zomba a Frank Matemba anayamikira Radio Maria kamba kowakonzera mbindikilowu umene wawathandiza kuti athe kuchita sitiko ya moyo wawo wa uzimu ndi kuyamba kuyendanso mu njira ya chipumumutso.