Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Komiti Yaku Parliament yoona za misewu Iyendera Msewu Wa Chingale.

$
0
0

Anthu a m’madera a mmaboma a Zomba, Machinga ndi Blantyre ati ndiokondwa kaamba ka kubwera kwa komiti yowona za misewu ya kunyumba ya malamulo yomwe inakayendera msewu wa Chingale umene wadutsira m’ma boma-wa.

Polankhula   ndi Radio Maria Malawi wapampando wa comiti-yi  a Victor Mbewe ati kimiti yawo inadzayendera msewuwu kamba kokhudzidwa ndi mavuto omwe anthu akupitilira kukomana nawo pa nkhani zokhudza mayendedwe.

Iwo ati komiti yawo iyesetsa kuti msewuwu ukonzedwe mwa changu.

Ena mwa amene anapezekanso pa mkumano woyendera maderawa ndi monga a episikopi a mpingo wakatolika mu dayosizi ya Zomba , ambuye  George Tambala, Bambo Henery Saindi omwe ndi mlembi wa mkulu wa bungwe la ma episikopi a mpingo wakatolika m’dziko muno ku ECM , komanso bambo Peter Mlomole omwe amaona zachitukuko mu dayosizi ya Zomba.         


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>