Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Achinyamata Apempha Boma Kuti Liwathandize Ndi Ndalama Zoyambira Business.

$
0
0

Achinyamata m’dziko muno ayamikira boma kamba kokhadzikitsa ntchito zosiyanasiyana zomwe zayamba kuthandiza pa ntchito zokweza achinyamata m’dziko muno.

Grace Scotch ndi amene wanena izi mwambo wa tsiku loganizira za achinyamata padziko lonse , umene umachitikira  pa bwalo la Manica m’boma la Balaka.

Grace Scotch amenenso amalankhula moyimira achinyamata onse m’dziko muno , anapitiliza ndi kunena kuti ngakhale boma likudzipeleka pa ntchito zokweza ntchito za achinyamata m’dziko muno , komabe zikuoneka achinyamata-wa akusowabe zambiri zowathandizira pa miyoyo yawo monga mpamba woyambira ma business, kuwathandiza pa maphunziro awo ndi zina zambiri.

Mlendo wolemekezeka ku mwambo-wu , anali mayi wa ku nyumba ya m’tsogoleri wa dziko lino , mayi Getrude Muthalika .

Iwo anati achinyamata akuyenera kupewa kuchita makhalidwe oyipa monga kusuta chamba kumwa mowa mwa uchidakwa, ndinso kukonda kulimbikitsa ziwawa mdziko muno ndi zina zambiri.

Iwo anati mwa zina achinyamatawa akuyeneranso kumadzisamalira ndi kuti asakhudzidwe ndi mulili wa matenda a edzi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>