Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Awapempha Kuti Akonzekere Bwino Chaka Cha Nkhoswe Ya Dayosizi Yawo.

$
0
0

Episikopi wa mpingo wakatolika mu dayosizi ya mangochi ambuye montfort Stima apempha akhristu mu dayosiziyo kuti akonzekere bwino pa tsiku la chaka cha nkhoswe ya dayosizi-yi.

Ambuye-wa alankhula izi pa msonkhano waukulu wokonzekera chakachi umene wachitika pa 26 August 2017  ku  Mangochi Cathedral .

Iwo ati akhristu akuyenera kukonzekera bwino chakachi ndi cholinga choti adzathe kukwanitsa kuthandiza dayosiziyo ndi chuma kapena katundu amene angathe kudzathandiza dayosiziyi pa tsikuli ndi cholinga choti ntchito zake zipitilire kuyenda bwino.

Polankhulanso moyimira akhristu ena ake a Steven Lingamawa anati ngati akhristu akonzekera bwino tsikuli ndi kuti lidzakhala lopambana .

Iwo atsimikizira mpingowu kuti komiti yawo iyowenetsetsa kulumikizana ndi akhristu onse a mingowu pa zaubwino wothandiza mpingo modzidalira.

Chaka cha nkhoswe ya dayosisi ya Mangochi chidzachitika pa 7 October chaka chino ku Mangochi Cathedral.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>