Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu ali ndi Udindo Woyezetsa Magazi

$
0
0

Anthu ati ali ndi udindo wokayezetsa magazi ndi cholinga choti adziwe momwe mthupi mwao mulili.

M’modzi mwa dotolo wa pa chipatala cha Mwaiwathu Dr.Simon Chiumia anena izi mu mzinda wa Blantyre pa msonkhano wa atolankhani omwe cholinga chake chinali kupereka uthenga woti anthu azikayezetsa magazi adakali amphamvu ndi cholinga choti mankhwala otalikitsa moyo azigwira bwino ntchito munthu akapezeka ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ka HIV.

Iwo ati padakali pano zinthu zasintha ndipo munthu akapezeka ndi kachilombo ka HIVakuyenera nthawi yomweyo kuyamba kumwa makhwala otalikitsa moyo.

“Aliyense akuyenera kuyezetsa ndi kuyamba kulandira mankhwala otalikitsa moyo nthawi yomweyo ngati wapezeka ndi kachilombo. Aliyense m’banja akuyenera ayezetse osati amayi okha kapena abambo okha ayi chifukwa ngati amayi alibe kachilombo sizikutanthauza kuti abambonso alibe,” anatero Dr. Chiumia.

Iwo ati chipatalachi chikupereka mwayi woti anthu akayezetse ndi kulandira malangizo mwa ulere ku chipatalachi komanso aziyenda m’malo osiyanasiyana kuti afikire anthu amene sakhala ndi nthawi yopita kuchipatala kukayezetsa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>