Bungwe la ma episikopia mpingo wakatolika m’dziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM) lati anthu m’dziko muno angachite bwino pa chitukuko cha miyoyo yawo ngati angachilimike pogwilitsa bwino ntchito zinthu zomwe ali nazo.
Mlembi wa bungwe-li bamboHenry Saindi ndi omwe anena izi pa m’buyo pa maphunziro achitukuko cha ulimi ndi zina a SummerInternationalSchool omwe bungwe-li linali nawo ku St. Johns, M’samba Parishi mu arch-dayosizi ya Lilongwe. Maphunziro-wa anali asabata imodzi.
Malingana ndi bambo Saindi mwa zina nthumwi zomwe zachita nawo maphunziro-wa zinachitanso ulendo wokayendera malo a ntchito za ulimi omwe bungwe la CADECOM likulimbikitsa alimi a mu Sikimu ya Chimutu m’dera la mfumu yayikulu Chimutu m’boma la Lilongwe.
“Tili ndi zonse zoziyenereza monga nthaka, madzi ndi zina zomwe zingatithandize kukhala oziyimira patokha. Tikagwiritsa ntchito zinthu zomwe tili nazo tikhala ozidalira pa chakudya komanso zokolora zomwezi akagulitsa amanga nyumba zabwino ndipo nyumba zake kukhala za magetsi a solar. Izi ndi zomwe tikulimbikitsa anthu akumudzi akhale ozidalira mu zonse,” anatero bambo Saindi.
Iwo ati ulendo-wu unakonzedwa ngati njira imodzi yokuzirannso maphunziro-wa.
Ku maphunziro-wo kunafika ma ena mwa episikopi a mpingo wakatolika , akulu-akulu a bungwe la CADECOM , ophunzira ku sukulu ya ukachenjede ya Catholic University ndi ena mu mpingo-wu.