Episikopi wa mpingo wakatolika mu dayosizi ya Mangochi olemekezeka Ambuye Montfort Stima wasankha bambo Frank Chingale kukhala Vicar General wa dayosizi-yi kuyambira pa 30 August 2017.
Padakalipano mkulu wa kuofesi ya zofalitsa nkhani ndi mauthenga osiyanasiyana mu dayosiziyo bambo Emmanuel Malipa afunira zabwino bambo-wa pomwe akhale akutumikira mpingo pa udindo-wu.
Iwo ati bambowa ngakhale asankhidwa kukhala nduna ya a episikopi a dayosizi akhala akupitilizabe kutumikira mpingowu ngati mkulu wa kuofesi yoona za maphunziro mu dayosiziyo.
Bambo Chingale asankhidwa pa undinowu polowa m’malo mwa malemu bambo Andrew Nkhata omwe anali Vilcar General a dayosiziyi