Msonkhano wa amayi a wakatolika mu dayosizi ya zomba wayamba pa 31 August 2017 ndipo udzatha pa 3 September 2017.
Polankhula potsekulira msonkhano-wu Episikopi wa mpingo wakatolika mu dayosizi-yi ambuye Gorge Desmond Tambala wayamikira m’gwilizano wa m’phamvu umene amayi-wa akuonetsa pa ntchito zotukula mpingo wakatolika mu dayosizi-yi.
Iwo alimbikitsa amayi-wa kuti pomwe akuchita mkumano-wu akumbukilenso kukambirana njira zothandizira kukwanilitsa mapulani a ntchito za chitukuko omwe dayosizi-yo yakhadzikitsa mchakachi.
Msonkhano wa bungwe la amayi achikatolika la Catholic Women Organisation (CWO) ukuchitira ku Thondwe Pastoral Center mu dayosiziyo ndipo udzatha la Mulungu pa 3rd September 2017.