Akhristu a mpingo wakatolika m’dziko muno awapempha kuti asamaope kukhala m’maudindo osiyanasiyana kamba koti kudzera m’maudindowa pomwe angathandize pa chitukuko cha dziko lino.
Bambo Hennery Chinkanda a ku Episcopal Conference Of Malawi (ECM) ndi omwe anena izi ku Limbe Catherdral pambuyo pa maphunziro a akhristu omwe ali ndi chidwi chofuna kutenga nawo mbari pa nkhani zokhudza ndale.
Iwo ati kuchita ndale sichimo koma kuti ndalezo zikuyenera kuchitika pofuna kuthandiza pa chitukuko cha dziko .