Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mariatona wa Lokolo Atsekulidwa pa 15 October

$
0
0

Mwambo wotsekulira Mariatona wa lokolo akuti udzachitika loweruka pa 15 mwezi uno ku likulu kwa Radio Maria Malawi ku Mangochi.

M’modzi mwa akulu akulu oyendetsa ntchito za Radio Maria Malawi a Emmanuel Kaliati atsimikiza za nkhaniyi.

Iwo ati mwambo wotsekulira Mariatona yu udzachitikansopamodzi ndi mwambo wotsekulira goloto ya Amai Maria yomwe yamangidwa ndi ndalama za Mariatona wa pa dziko lonse yemwe anachitika m’mwezi wa Julychakachino.

“Mariatona aliponso ndipo uyu ndi wa lokolo pamene watha uja anali wa international. Pamene tikutsekulira mariatona ameneyu titsekuliranso goroto la Amai Maria yomwe yamangidwa ndi ndalama zomwe tinapeza pa mariatona wa international watha uja,” anatero a Kaliati.

Iwo ati Mariatona wa lokoloyu cholinga chake ndi chofuna kumanga nyumba ya nthambi ya Radio Maria ya Limbe yomwe padakali pano imakhala mu nyumba ya arkidayosizi ya Blantyre.

Iwo anati, “Tithokoze a arkidayosizi kaamba kotilora kumakhala mu nyumba mwawo mwaulere koma tsopano tawona kuti Radio Maria ikhale ndi nyumba yakeyake ya sub studio imeneyi. Ndiye Radio Maria siingathe kumanga yokha nyumbayi koma ikudalira thandizo la omvera ake.”

A Kaliati apempha abwenzi komanso omvera onse a wailesiyi kuti atengepo gawo lalikulu pothandiza wailesiyi pa ntchitoyi kudzera mu Mariatona yu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko