Bwalo loyamba lamilandu m’boma la Mwanza lalamula mwamuna wina wa zaka 28 zakubadwa kuti akakhale kundende kwa zaka 10 kaamba kopezeka olakwa pa mulandu wogwililira mwana wa msungwana wa zaka 15 zakubadwa.
Malinga ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergeant Edwin Kaunda mwamunayu Kashoni Masauko pa 22 July chaka chino anagwilira mwanayu panthawi yomwe amapita kukatunga madzi ku mjigo.
Pamenepa a Kashoni akuti anamunyengerera nsungwanayu ndi ndalama yokwanira 5 sausande kwacha cholinga choti asakaulure pa zomwe zachitikazo koma akuti msungwanayu anakawauza mayi ake. malipoti achipatala chaching’ono cha Tulonkhondo anatsimikiza kuti msungwanayu anagwiriridwadi.
Popereka chigamulo chake His Worship Ranwel Mangazi anati wapereka chigamulo cha mtunduwu kuti anthu ena atengerepo phunziro.
A Kashoni Masauko amachokera m’mudzi wa a Jekapu kwa mfumu yaikulu Chiwere m’boma la Dowa.