Apolisi ku Lumbadzi m’boma la Dowa akusunga m’chitolokosi bambo wina wa zaka 22 zakubadwa kamba kopezeka ndi ndalama zachinyengo.
Malingana ndi wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za polisi ku kanengo mu m’dzinda wa Lilongwe a Salome Chibwana ati bamboyu ndi Chione Apatsamosiyana ndipo amachokera m’mudzi mwa Kadzakamba m’dera la mfumu yayikulu Chakhadza m’boma la Dowa ndipo akaonekera ku bwalo lamilandu ndi kukayankha mulandu wopezeka ndi ndalama zachinyengo .