A Kulikulu la mpingo wakatolika m’dziko muno ku EPISCOPAL CONFERENCE OF MALAWI (ECM) alengeza za imfa ya bambo WILLEM WESTER omwe akhala akutumikira mpingowu ku ARCH DAYOSIZI ya Blantyre
Bambo Wellem Wester anamwalira m’mawa wa tsiku lachisanu pa 8 SEPTEMBER 2017 ku chipatala cha ADVENTIST mu m’zinda wa BLANTYRE komwe amakalandira thandizo la mankhwala atazindikira kuti sanali kupeza bwino m’thupi mwawo. Iwowa anali mbadwa ya dziko la NERTHERLANDS , ndipo anabadwa mchaka cha 1927 ndipo anadzozedwa unsembe mchaka cha 1957.
Malemu bambo WESTER atumikira m’maparish a Neno, Nguludi, Muona, Molere, KonzaAlendo, Nkhate, Bango, Njuli ndi ena ambiri kuyambira mchaka cha 1958 ndipo anapuma pa ntchitoyi kuyambira mchaka cha 2014.
Mwambo woyika m’manda thupi la malemu Bambo WESTER uchitika Loweruka pa 9 SEPTEMBER 2017 ku manda a ansembe ku NAMTIPWIRI kwa BVUMBWE m’boma la THYOLO . Mwambowu udzayamba ndi Nsembe ya misa yaulemu yomwe adzatsogolere ndi wolemekezeka Ambuye THOMAS LUKE MSUSA omwe ndi EPISIKOPI wa ARCH-DAYOSIZI ya BLANTYRE. Bambo Wester anali A chipani cha MONTFORT MISSIONARIES ndipo atisiya ali ndi zaka 90 zakubadwa.