Bungwe lopereka magazi la MALAWI BLOOD TRANSFUNSION SERVICE (MBTS) layamikira anthu a m’boma la Ntcheu kaamba kodzipereka pantchito yopereka magazi pamene bungweli limagwira ntchito yotolera magazi m’madela ena m’bomali
Malingana ndi m’kulu woyang’anira ntchito yopereka magazi m’bomali a ZIONE CHIMALIZENI, Iwo ati kuonetsa chidwi pa ntchito yopereka magazi zimasonyeza kuti munthu akumvetsa bwino cholinga cha bungweli.
Pamenepa a Chimalizeni apempha anthu mdziko muno kuti adzikonda kupereka magazi kuti dziko lino lipulumutse miyoyo ya nthu omwe amasowa magazi mzipatala zosiyanasiayana.