Akhristu amene ali pa ulendo wa ku malo oyeraa KIBEHO m’dziko la RWANDA awapemphaakuti asadere nkhawa pa zaulendowu kaamba koti zomwe achitazi ndi zopambana mu mbiri ya moyo wawo wa chikhristu. Izi analankhula ndi Wachiwiri kwa wapampando wa bungwe lomwe lakonza ulendowu la DEVINE MERCY APOSTOLATE a OSWARD BWEMBA.Iwo ati aliyense amene wayenda pa ulendowu sikuti wataya ndalama koma kuti wasonkhozera madalitso ochuluka pa moyo wake wa chikhristu.
Akhristu a mpingo wakatolikawa anyamuka lachisanu pa 8 SEPTEMBER 2017 kupita m’dziko la RWANDA , komwe akhakhaleko sabata imodzi ndi kubwelera kuno ku mudzi pa 17 mwezi uno ndipo akhristu pafupifupi 35 ndi omwe akuyenda nawo pa ulendowu.