Quantcast
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Alimbikitsa Ubale wa Pakati pa Mpingo Wakatolika ndi Anglican

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha akhristu a mpingo wa katolika ndi Anglican kuti azigwilira ntchito limodzi ndi cholinga chofuna kulimbikitsa umodzi pakati pawo.

Papa amalankhula izi pa nkumano omwe anali nawo ndi mkulu wa mpingo wa Anglican Archbishop of Canterbury Justin Welby yemwe anakayendera likulu la mpingo wakatolika ku Vatican.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Papa wati ngakhale mipingo iwiriyi ili yosiyana koma cholinga chawo ndi chimodzi chofalitsa uthenga wabwino.

Papa anauzanso ma episkopi omwe anali nawo pa msonkhanowo kuti atsatire chitsanzo cha Yesu Khristu chothandizana pa mavuto ndi cholinga choti aziyendera limodzi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>