Anthu asanu ndi ena atatu (8) afa ndipo ena avulala modetsa nkhawa mini-bus yomwe anakwera itagubuduzika ku Nguludim’boma la Chiladzulu.
Malinga ndi m’modzi mwa omwe apulumuka pa ngoziyo mai Annie Thawale, anati mini-busi-yo yomwe imathamanga kwambiri inagubuduzika potsatira kuphulika kwa tayala. Mai thawale anafotokozera mtolankhani wathu Luke Chimwanza ndipo anati izi zinali chomwechi kaamba ka liwiro lochuluka lomwe Dalaivala wa Mini Busi-yo amafuna kudutsa ena mwa magalimoto omwe amayenda pa msewupo.
Ndipo ati ali mkati mwa liwilori tayala la galimotoyo linaphulika zomwe zinapangitsa kuti galImotoyo igubuduzike katatu ndipo anthu okwana asanu komanso ena atatu anafera pa malo pomwepo komanso ena anamwalilira mu njira pa nthawi yomwe amapita nawo ku chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth Central Hospital.