Mpingo wakatolika mu Arch-Diocese ya Blantyre wapempha akhristu ake kuti ayendere limodzi ndi atumiki awo padongosolo lokonzanso masomphenya a mmene dayosiziyi iyendere zaka zisanu zikubwerazi.
Bambo Alfred Chaima omwe ndi mlembi owona zochitikachitika mu archi dayosiziyi ndi omwe alankhula izi ndi Radio Maria Malawi mu m’zinda wa Blantyre.
Iwo ati ngati Arch-Diocese akuyembekezera kuti akhristu-wa athandiza popereka ndemanga ndi maganizo za mmene mpingo uyendere mu nthawi yomwe yaikidwa