Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Francisco Wayamikira Ansembe Anayi A Mziko La United States Of America.

$
0
0

M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse papa Francisco wayamikira ansembe anayi omwe achita bwino pa mpikitsano wa ophunzira a msukulu za ukachenjede zomwe akhala akuphunzira m’dziko la United States Of America.

Malipoti a wailesi ya Vatican atsimikizira za nkhaniyi ndipo ati bungwe la Joseph Ratzinger Foundation ndilomwe linachititsa mpikitsanowu pofuna kulimbitsa ophunzira wa kuzama pa maphunziro awo.

Ansembewa omwe ndi Darcia Narvaez ochokera ku Notre dame University, Michael Schuck, Nancy C. Tuchmun ndi bambo Michael j. Garanzini achipani cha Jesuit kuchokera ku Loyola University.

Pamapeto pake mtsogoleri wa mpingo mwakatolikayu anati izi zilimbikitsa kupititsa patsogolo ntchito ya maphunziro komanso kutumikira mulungu mwaluntha komanso mwachilimbikitso.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>