Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Galimoto Lapsa M’boma la Dowa

$
0
0

Galimoto la mtundu wa truck m’boma la Dowa ati lapsa potsatira ngozi yomwe galimotoli lachita pafupi ndi msika wa Chakhungu m’bomalo.

Malinga ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali SergeantRichard Kaponda galimotoli nambala yake SA7019lomwe limachokera ku Lilongwe kupita ku Salimandipo limayendetsedwa ndi a Emmanuel Khoma a zaka 36 zakubadwa omwe anali ndi dalaivala nzawo mu galimotolo.

Sergent Kaponda ati galimotoli linanyamula matumba 3 hundred a cement ndipo pa nthawi yomwe imayandikira pa msikawu dalaivalayo anawona kuti tayala limodzi likuyaka moto.

Dalaivalayo pamodzi ndi mzakeyo ati anakwanitsa kutuluka mu galimotolo ndi kuyamba kufuula kupempha anthu kuti awathandize ndipo anthu omwe anafika pamalopo anakwanitsa kupulumutsa matumba ochepa a cement yo.

Iwo ati galimotolo lapseratu ndipo padakali pano apolisi m’bomalo akufufuza chomwe chinayambitsa motowo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>