Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

MABUNGWE AKWIYA NDI KUYIMITSIDWA KWA NTCHITO YOWUNIKA MAYINA MKAWUNDULA

$
0
0

Anthu komanso mabungwe omwe sia boma ati sakugwirizana ndi zomwe bungwe la za chisankho la MEC lachita poyimitsa ntchito ya mugawo loyamba lowunika mayina mukawundula wa voti yomwe inayamba lolemba mchigawo chakumpoto ndi m’madera ena amchigawo chapakati.

Polengeza izi kudzera mchikalata mkulu wowona za chisankho ku bungwe la MEC a Willie Karonga ati izi zachitika ntchitoyi itakumana ndi mavuto ochuluka maka m’maboma a Ntcheu, Mzimba, Nkhata Bay, Salima, Kasungu, Dedza komanso mzinda wa Mzuzu.

Malinga ndi a Karonga ntchitoyi inachedwa kuyamba m’malo ena kamba koti banki yaikulu mdziko muno ya Reserve inachedwa kuvomereza ndalama za bungweli komanso chifukwa cha mavuto a kuvuta kwa mayendedwe m’maboma ena kuzanso ena okhudza  kaundula wa votiyu.

‘’Ntchitoyi tayiyimitsa pofuna kuwonesetsa kuti ntchito zonse zokhudza chisankhochi ziyende bwino monga mukudziwa kuti tili ndi udindo wowonesetsa kuti chisankhochi chidzayende mwa ufulu komanso movomerezeka. Malo onse omwe ntchitoyi imachitikira atsekedwa ndipo tilengeza masiku atsopano omwe ntchitoyi izayambenso,’’ atero a Karonga.

Polankhulapo wapampado wa bungwe la Malawi Electoral Support Network a Steve Duwa ati ndi kofunika kuti bungweli lilongosole momveka bwino zifukwa zomwe layimitsira ntchitoyi.

‘’Ngati bungwe la MEC sililongosola momveka bwino pakhala nkhawa zoti likufuna kubera mavoti. Tikudabwa kuti mchifukwa chani bungwe la MEC silinakonzeke pamene limayamba ntchito imeneyi. Ntchito yowunika mayina mukawundula ndi yofunikira kwambiri pa chisankho ndipo zovuta ngati izi ndizozetsa chikayiko chachikulu ngati bungweli lili lokonzeka kuchititsa chisankho pa 20 May,’’ atero a Duwa. 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>