Maiko ena pa dziko lapansi adzudzula mtsogoleri wa dziko la America, Donald Trump kaamba ka ganizo lake lopanga mzinda wa Yerusalemu kukhala likulu la dziko la Israel.
Malipoti a wailesi ya BBC ati dziko la Saudi Arabia lati izi ndi zosamveka komanso zosavomerezeka pamene dziko la France komanso United Kngdom (UK) ati sakugwirizana ndi ganizolo.
Malipoti ati Trump wapanga izi mokomera dziko la America komanso ngati njira imodzi yodzetsa mtendere pakati pa dziko la Israel ndi Palestinapamene pali mpungwepungwe wosatha pakati pa maiko awiriwa.
Padakali pano Trump walamula kuti ofesi ya kazembe wa dziko la America mdzikolo isamuke kuchoka ku Tel Aviv lomwe ndi likulu lakale la dzikolo kupita ku mzinda wa Yerusalem.
Koma polankhulapo nduna yaikulu ya dziko la Israel a Benjamin Netanyahu ati iyi ndi mbali imodzi ya mbiri ya dzikolo ndipo ati akukhulupilira kuti mayiko ena atsatiranso ganizolo posamutsa ma ofesi a kazembe a maiko awo kupita mu mzinda wa Yerusalemu.
Ngakhale mkuluyu sanatchule maiko omwe ali pambuyo pa ganizolo kma malipoti akusonyeza kuti maiko a Phillipines komanso Czech Republic ndi omwe achite izi.