Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Awiri Afa pa Ngozi ya pa Nsewu mu Mzinda wa Lilongwe

$
0
0

Anthu awiri afa pa ngozi ya pansewu yomwe yachitika pafupi ndi Area 25 Filling Station mu mzinda wa Lilongwe.

Wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za a polisi pa polisi ya Kanengo mu mzindawo, Constable Salome Zgambo Chibwana, wauza Radio Maria Malawi kuti bambo wina, James Msiska yemwe amayendetsa galimoto la mtundu wa Saloon Opa nambala yake BR6337 amathamanga kwambiri zomwe zinachititsa kuti apite mbali ina ya nsewu komwe anakawomba galimoto lina la mtundu wa Toyota Passo nambala yake BS1267 lomwe limayendetsedwa ndi a Essau Chinyama.

Zitachitika izi a James Msiska komanso mayi wina yemwe sakudziwika yemwe anakwera naye mu galimotolo anakafera ku chipatala cha Kamuzu Central pamene woyendetsa wa galimoto linalo wavulala kwambiri m’mutu ndipo amugoneka pa chipatala chomwechi komwe akulandira chithandizo ndipo galimoto ziwirizi zawonongeka kwambiri.

Ngozi inanso yachitika pa msika wa Mthyoka mu nsewu wa Lilongwe-Salima pamene galimoto lina nambala yake MDF 802 yawombana ndi galimoto lina la mtundu wa truck nambala yake T350.

Anthu omwe anakwera mu galimotozi avulala kwambiri ndipo galimotozo zawonongekanso modetsa nkhawa.

Potsatira ngozi ziwirizi apolisi mu mzindawu akupempha madalaivala onse a galimoto kuti azitsatira malangizo a pa nsewu komanso kuwona zikwangwani kuti apewe ngozi zomwe zikanatha kupeweka.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>