Mamembala a gulu lakale la boma la Malawi Young Pioneers [MYP] lachiwiri anakatula chikalata kwa pulezidenti Joyce Banda kudzera ku ofesi ya bwanamkubwa wa mboma la Lilongwe chopempha kuti alowererepo pa nkhani zokhudza malipiro awo.
Gulu la achinyamata la Malawi Young Pioneers linathetsedwa mchaka cha 1993 kudzera ku ntchito yotchedwa Operation Bwezani yomwe asilikali adziko lino anayikhazikitsa pomwe anamenyana ndi kubalalitsa mamembala a gululi m’malo onse omwe amagwirira ntchito zawo mdziko muno.
Mwa zina kalatayo yomwe yasainidwa ndi mamembala akuluakulu asanu ndi atatu ikupempha kuti maofesi a mlembi wamkulu waboma, mlembi woona zolemba anthu ntchito m'boma, mkulu owerengera chuma ndiponso mkulu owona zopereka ndalama kwa anthu omwe apuma pantchito awafufuze bwino pa malipoti onena kuti anasakaza ndalama za chipukuta misonzi zomwe mamembala a MYP amayenera kulandira.
‘’Tinatsatira ndondomeko zonse pokambirana ndi akulu akulu amenewa kuti aleke kugwira ntchito ndi komiti yomwe inalipo yomwe inachititsa kuti anthu olakwika alandire ndalama zomwe ife timaenera kulandira,’’ chatero chikalatacho.
Mlembi wofalitsa nkhani za gululi yemwenso analankhulira mamembalawo a Hendrix Chijota ati anthu ena achinyengo omwe simamembala agululi analandira ndalama zochuluka.
‘‘Tinachotsedwa ntchito nthawi yathu isanakwane koma koma ndalama zomwe anakonza kuti anthu azilandira ndizochepa kwambiri mukhoza kuganiza kuyambira mchaka cha 1993 tizilandira ndalama zokwana K1500 ngati opuma pa ntchito,’’atero a Chijota.
A Chijota ati akufunanso chilungamo potsatira nkhanza zomwe analandira pomwe amayi amgululi anagwiliridwa pamaso pa ana awo komanso potsatira kuphedwa kwa anzawo pa nthawi ya Operation Bwezani pomwenso katundu wawo anawonongeka.
Poyankhula atalandira chikalatacho mmalo mwa bwanamkubwa wa mboma la Lilongwe, mkulu woyang’anira ntchito za khonsolo ya mbomalo a Peter Dokali anayamikira mamembalawo chifukwa chopereka chikalatacho mwa bata ndipo anatsimikizira a Payoniyawo kuti chikalatacho achipereka kwa Pulezidenti Joyce Banda kudzera ku ofesi ya pulezidenti ndi nduna.