Mkulu wa apolisi m’chigawo cha ku m’mawa kwa dziko lino Commissioner Effie Kaitano wathokoza mafumu, anthu akumudzi komanso apolisi eni ake kaamba kogwirana manja pa ntchito yochepetsa umbava ndi umbanda m’chigawochi m’chaka cha 2016.
Commissioner Kaitano amalankhula izi ku sukulu ya sekondale ya Mulunguzi m’boma la Zomba pa phwando la chaka chatsopano lomwe anakonzera akuluakulu a polisi m’chigawochi.
Iwo ati pakadali pano anthu a khungu la chi alubino akuyenda mopanda mantha kaamba ka mgwirizano wa pakati pa apolisiwa ndi anthu akumudzi.
Pamenepa iwo ati ayesetsa kuti apolisi azipezeka paliponse ndi cholinga chofuna kupitiriza kupereka chitetezo chokwanira.
Mkulu wowona za ntchito ku likulu la polisi mdziko muno Senior Deputy Commissioner Joseph Chabuluka yemwe anafika kumwambowu m’malo mwa mkulu wa apolisi mdziko muno wati sadzalekelera wapolisi aliyense wochita zaumbanda kapena kugwirizana ndi okuba m’malo mopereka chitetezo kwa anthu ndipo anati apolisi oterowo adzachotsedwa ntchito.