Achinyamata a mpingo wa katolika mdziko muno awapempha kuti atengepo mbali pothandiza anthu okalamba komanso osowa mdziko muno.
Wachiwiri kwa wapampando wa gulu la achinyamata a ku tchalitchi la St. Marys Namame yomwe ndi nthambi ya parishi ya Limbe mu arkidayosizi ya Blantyre, Tadala Stranger ndi yemwe wanena izi pamene gululi linakayendera ndi kupereka thandizo kwa agogo ena opezeka kwa mfumu yaikulu Kapeni m’boma la Blantyre. Iye wati achinyamatawa achitanso izi ngati njira imodzi yokonzekera kubadwa kwa yesu khristu pamene mpingo wa katolika padakali pano uli mu nyengo ya Advent.
Polankhulapo, m’modzi mwa agogo omwe alandira thandizolo gogo Peter Billiati ayamikira achinyamatawa kaamba ka thandizolo ndipo awapempha kuti apitirize kutumikira mpingo modzipereka.