Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Obama Apempha Anthu Ateteze Ufulu Wa Democracy

$
0
0

Mtsogoleri wopuma wa dziko la America, Barrack Obama wapempha anthu m’dzikolo kuti akhale oteteza ufulu wa dimokalase.

Malipotia wailesi yaBBCatiObamaamalankhula izi mu mzinda wa Chicago kudzera mu uthenga wake wotsanzikana ndi anthu pa udindowu.

Iye anati padakali pano dziko la America ndi losinthika poyerekeza zaka zisanu ndi zitatu 8 zapitazo pamene anayamba kulamulira dzikolo koma anachenjeza anthu kuti alemekeze ufulu wa demokalase-wu.

Iye anati kusinthana mpandowu mwamtendere ndi a Donald Trump ndi chitsimikizo chachikulu cha ufulu wa demokalase komabe anati dzikolo lili pa mavuto a tsankho pa nkhani za chuma, tsankho la mitundu ya anthu komanso kugawikana kwa madera.

Mtsogoleri wa dziko la America woyamba wachikudayu amene ali ndi zaka 55 anasankhidwa kukhala pulezidenti wa dzikolo m’chaka cha 2008.

Mlowam’malo wake Donald Trump wati akuyembekezeka kusintha zina zomwe Obama ankachita mdzikolo akalumbiritsidwa kukhala pulezidenti wa dzikolo pa 20 mwezi uno.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>