Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

ANC Ikuyembekezeka Kusankha Mlowam’malo wa Zuma

$
0
0

Akuluakulu a chipani cholamula mdziko la South Africa cha African National Congress (ANC) akukonza zopeza mtsogoleri watsopano wa chipanichi yemwe atalowe m’malo mwa mtsogoleri wa dzikolo Jacob Zuma.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, pakadalipano anthu amene akupikisana pa udindowu ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikolo a Cyril Ramaphosa komanso Mkosazana Dlamini-Zuma yemwe ndi nduna yakale komanso mkazi wakale wa mtsogoleri wa dzikolo a Jacob Zuma.

Amene atapambane, ali ndi kuthekera kolowa m’malo mwa a Zuma ndi kukhala mtsogoleri wa dzikolo koma pali chiwopsezo kuti chipanichi chitha kugawikana isanafike nthawi ya chisankho chomwe chichitike mchaka cha 2019.

A Zuma apitilirabe kukhala mtsogoleri wa dzikolo kufikira nthawi ya chisankhocho.

President Zuma wakhala pa udindowu kuyambira chaka cha 2009 ndipo dziko la South Africa limalola munthu kukhala mtsogoleri wa dzikolo kwa materemu awiri a zaka zisanu iliyonse.

Pa mkumano womwe akuluakulu a chipanicho anali nawo, a Zuma omwe padakali pano akukhudzidwa ndi nkhani za katangale mdzikolo, apempha anthu mchipanicho kuti agwire ntchito ndi aliyense mwa awiriwa yemwe atasankhidwe kukhala mtsogoleri wa chipanicho.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>