Apolisi m’boma la Mangochi akusunga mchitikosi amuna anayi powaganizira kuti akukhudzidwa ndi kubedwa kwa mu shop ina ya mzika ya dziko la Rwanda m’bomalo.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Inspector Rodrick Maidawauza Radio Maria Malawi kuti pa 15 December amanga Gift Sitamba wa zaka 29 zakubadwa ndipo amupeza ndi mfuti komanso zipolopolo ziwiri.
Pa 16 December agwira Thomas Useni wa zaka 28 zakubadwa ndipo patsiku lomweli anagwiranso Aliseni Alli yemwe amupeza ndi mufti komanso zipolopolo khumi ndi zitatu 13.
Ndipo pa 18 December ndi pomwe amanga Muhamad Alli wa zaka 32 zakubadwa yemwe amugwilira ku Biliwiri m’boma la Ntcheu pa ulendo wake wopita mdziko la South Africa.
Amunawa akuwaganizira kuti pa 13 December chaka chino anawopseza mwini wa shop ina ndi kuba ndalama zokwana 124, 000 kwacha, maunitsi a ndalama zokwana 15 000 kwacha ndipo anawombera amuna awiri omwe amafuna kuwagwira pa nthawi yi.
Pakadali pano zinthu zomwe zapezeka ngati umboni wa ku khothi ndi ndalama zokwana 3000 kwacha, mayunitsi a ndalama zokwana 8000 kwacha, mifuti iwiri, ma magazine atatu komanso zipolopolo 18.
Apolisi m’bomali athokoza anthu omwe athandiza kuti mbavazi zomwe zikawonekere ku bwalo la milandu posachedwapa, zigwidwe.